Acts 15:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tamva kuti anthu ena ochokera m'gulu lathu akhala akukuvutani ndi kukusokonezani maganizo. Amenewo sitidaŵatume ndife ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza tamva kuti ena amene anatuluka mwa ife anakuvutani ndi mau, nasocheretsa mitima yanu; amenewo sitinawalamulira;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ife tamva kuti anthu ena ochokera pakati pathu, amene sitinawatume anakusokonezani maganizo ndi kukuvutitsani ndi zimene amakuwuzani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza tamva kuti ena amene anaturuka mwa ife anakubvutani ndi mau, nasoceretsa mitima yanu; amenewo sitinawalamulira;