Acts 15:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mpingo utaŵatuma, adadzera ku Fenisiya ndi Samariya akufotokoza za m'mene anthu osakhala Ayuda adatembenukira mtima. Mau ameneŵa adakondweretsa abale onse kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo anaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Fenisiya ndi Samariya, nafotokozera chisanduliko cha amitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mpingo unawaperekeza, ndipo pamene amadutsa ku Foinike ndi Samariya, iwo anafotokoza momwe a mitundu ina anatembenukira mtima. Nkhani imeneyi inakondweretsa kwambiri abale onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo anaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Foinike ndi Samariya, nafotokozera cisanduliko ca amitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse.