Acts 15:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene adafika ku Yerusalemu, adalandiridwa ndi mpingo ndi atumwi ndi akulu a mpingo. Paulo ndi Barnabasi adaŵafotokozera ntchito zonse zimene Mulungu adaachita mwa iwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene anafika ku Yerusalemu, analandiridwa ndi Mpingo, ndi atumwi ndi akulu, ndipo anabwerezanso zonse zimene Mulungu anachita nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika ku Yerusalemu, iwo analandiridwa ndi mpingo, pamodzi ndi atumwi ndiponso akulu ampingo. Paulo ndi Barnaba anawafotokozera zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene anafika ku Yerusalemu, analandiridwa ndi Mpingo, ndi atumwi ndi akuru, ndipo anabwerezanso zonse zimene Mulungu anacita nao.