Acts 15:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma okhulupirira ena amene kale anali a m'gulu la Afarisi, adaimirira nati, “Nkofunika kuti okhulupirira a mitundu ina aumbalidwe, ndiponso aŵalamule kuti azitsata Malamulo a Mose.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anauka ena a mpatuko wa Afarisi okhulupirira, nati, Kuyenera kuwadula iwo, ndi kuwauza kuti asunge chilamulo cha Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka, okhulupirira ena amene kale anali a gulu la Afarisi anayimirira ndipo anati, “Anthu a mitundu ina ayenera kuchita mdulidwe ndi kusunga malamulo a Mose.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anauka ena a mpatuko wa Afarisi okhulupira, nati, Kuyenera kuwadula iwo, ndi kuwauza kuti asunge cilamulo ca Mose.