Acts 15:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atakambirana nthaŵi yaitali, Petro adaimirira naŵauza kuti, “Abale anga, mukudziŵa kuti pa masiku oyamba aja Mulungu adandisankha ine pakati pa inu kuti ndilalike Uthenga Wabwino kwa anthu a mitundu ina, kuti amve ndi kukhulupirira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene panali mafunsano ambiri, Petro anaimirira, nati kwa iwo, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu anasankha mwa inu, kuti m'kamwa mwanga amitundu amve mau a Uthenga Wabwino, nakhulupirire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atakambirana kwambiri Petro anayimirira, ndipo anawayankhula nati: “Abale, mukudziwa kuti masiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu kuti anthu a mitundu ina amve kuchokera pakamwa panga mawu a Uthenga Wabwino ndi kukhulupirira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene panali mafunsano ambiri, Petro anaimirira, nati kwa iwo, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu anasankha mwa inu, kuti m'kamwa mwanga amitundu amve mau a Uthenga Wabwino, nakhulupire.