Acts 16:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye ataona zimenezi, nthaŵi yomweyo tidakonza ulendo wopita ku Masedoniya, chifukwa tidaadziŵadi kuti Mulungu ndiye watiwongolera kuti tikaŵalalikire Uthenga Wabwino anthu akumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene anaona masomphenyawo, pomwepo tinayesa kutulukira kunka ku Masedoniya, poganizira kuti Mulungu anaitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paulo ataona masomphenyawa, tinakonzeka kupita ku Makedoniya, kutsimikiza kuti Mulungu anatiyitana kuti tikalalikire Uthenga Wabwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene anaona masomphenyawo, pomwepo tinayesa kuturukirakunka ku Makedoniya, poganizira kuti Mulungu anaitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo.