Acts 16:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuchokera kumeneko tidapita ku Filipi, mzinda wa m'chigawo choyamba cha m'dera lija la Masedoniya, ndiponso boma la Aroma. Tidakhala mu mzinda umenewo masiku angapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pochokera kumeneko tinafika ku Filipi, mudzi wa ku Masedoniya, waukulu wa m'dzikomo, wa milaga ya Roma; ndipo tidagona momwemo masiku ena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera kumeneko tinapita ku Filipi, boma la Aroma ndiponso mzinda waukulu wa dera la Makedoniya. Tinakhala kumeneko masiku owerengeka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pocokera kumeneko tinafika ku Filipi, mudzi wa ku Makedoniya, waukuru wa m'dzikomo, wa miraga ya Roma; ndipojidagona momwemo masiku ena.