Acts 16:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakati pao padaali mai wina, dzina lake Lidia. Anali wa ku mzinda wa Tiatira, ndipo ntchito yake inali yogulitsa nsalu zofiirira. Anali munthu wopembedza Mulungu, ndipo Ambuye adaatsekula mtima wake kuti azisamale zimene Paulo ankanena.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatimva mkazi wina dzina lake Lidia, wakugulitsa chibakuwa, wa kumudzi wa Tiatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wake Ambuye anatsegula; kuti amvere zimene anazinena Paulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmodzi wa amayi amene amamvetserawo ndi Lidiya amene amagulitsa nsalu zofiira, wochokera ku mzinda wa Tiyatira, ndipo amapembedza Mulungu. Ambuye anatsekula mtima wake kuti amve mawu a Paulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatimva mkazi wina dzina lace Lidiya, wakugulitsa cibakuwa, wa ku mudzi wa Tiyatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wace Ambuye anatsegula, kuti amvere zimene anazinena Paulo.