Acts 16:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ambuye ake a mtsikana uja ataona kuti sangapindule nayenso, adagwira Paulo ndi Silasi naŵakokera ku bwalo, kwa akulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene ambuye ake anaona kuti kulingalira kwa kupindula kwao kwatha, anagwira Paulo ndi Silasi, nawakokera kunka nao kubwalo kwa akulu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ambuye a mtsikana uja anazindikira kuti chiyembekezo chawo chopezera ndalama chatha, anagwira Paulo ndi Sila nawakokera ku bwalo la akulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene ambuye ace anaona kuti kulingalira kwa kupindula kwao kwatha, anagwira Paulo ndi Sila, nawakokera kunka nao kubwalo kwa akuru,