Acts 16:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Woyang'anira ndende uja atadzuka, naona kuti zitseko zonse za ndende nzotsekuka, adaayesa kuti akaidi athaŵa. Pamenepo adasolola lupanga lake nati adziphe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene anautsidwa kutulo mdindoyo, anaona kuti pa makomo a ndende panatseguka, ndipo anasolola lupanga lake, nati adziphe yekha, poyesa kuti am'ndende adathawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Woyangʼanira ndende uja atadzuka ku tulo, anaona kuti zitseko za ndende zinali zotsekula, ndipo anasolola lupanga lake nafuna kudzipha chifukwa ankaganiza kuti amʼndende athawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene anautsidwa kutulo mdindoyo, anaona kuti pa makomo a ndende panatseguka, ndipo anasolola lupanga lace, nati adziphe yekha, poyesa kuti am'ndende adathawa.