Acts 16:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Paulo adafuna kuti iye amperekeze. Tsono adamuumbala chifukwa cha Ayuda amene anali kumeneko, pakuti onse ankadziŵa kuti bambo wa Timoteo ndi Mgriki.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iyeyo Paulo anafuna kuti amuke naye, ndipo anamtenga, namdula, chifukwa cha Ayuda amene anakhala m'maikomo; pakuti onse anadziwa kuti atate wake anali Mgriki.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paulo anafuna kumutenga pa ulendo, kotero anachita mdulidwe chifukwa cha Ayuda amene amakhala mʼderalo pakuti onse amadziwa kuti abambo ake anali Mgriki.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iyeyo Paulo anafuna kuti amuke naye, ndipo anamtenga, namdula, cifukwa ca Ayuda amene anakhala m'maikomo; pakuti onse anadziwa kuti atate wace anali Mhelene.