Acts 16:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Paulo adauza asilikaliwo kuti, “Iwo aja adatikwapulira pa anthu, osaweruza mlandu wathu, chonsecho ndife nzika za ufumu wa Aroma, kenaka nkutiponya m'ndende. Ndiye tsopano akufuna kutitulutsa mobisa? Izo ndizo ai! Abwere iwowo adzatitulutse okha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Paulo anati kwa iwo, Adatikwapula ife pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ife amene tili Aroma, natiika m'ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutitulutsira ife m'tseri? Iai, ndithu; koma adze okha atitulutse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Paulo anati kwa asilikaliwo: “Iwo anatikwapula pa gulu la anthu asanatiweruze, ngakhale kuti ndife nzika za Chiroma natiponya mʼndende. Kodi tsopano akufuna kutitulutsa mwamseri? Ayi! Asiyeni abwere okha kuti adzatitulutse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Paulo anati kwa iwo, Adatikwapula ire pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ire amene tiri Aroma, natiika m'ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutiturutsira ire m'tseri? Iai, ndithu; koma adze okha atiturutse.