Acts 16:38 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asilikali aja adapita kukaŵafotokozera akulu oweruza milandu aja mau ameneŵa. Pamene iwo aja adamva kuti ndi nzika za ufumu wa Aroma, adachita mantha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akapitao anafotokozera mauwo kwa oweruza; ndipo iwowo anaopa, pakumva kuti anali Aroma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asilikali aja anakafotokozera woweruza milandu ndipo pamene anamva kuti Paulo ndi Sila anali nzika za Chiroma, anachita mantha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akapitao anafotokozera mauwo kwa oweruza; ndipo iwowo anaopa, pakumva kuti anali Aroma.