Acts 16:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usiku Paulo adaona m'masomphenya munthu wina wa ku Masedoniya ataima nkumampempha kuti, “Olokerani ku Masedoniya kuno, mudzatithandize.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Panali munthu wa ku Masedoniya alinkuimirira, namdandaulira kuti, Muolokere ku Masedoniya kuno, mudzatithangate ife.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi ya usiku Paulo anaona masomphenya, munthu wa ku Makedoniya atayimirira ndi kumupempha kuti, “Bwerani ku Makedoniya, mudzatithandize.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Panali munthu wa ku Makedoniya alinkuimirira, namdandaulira kuti, Muolokere ku Makedoniya kuno, mudzatithangate ife.