Acts 17:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti pamene ndinalikuyenda mumzindamu, nkumaona malo anu osiyanasiyana achipembedzo, ndinapezanso guwa lina lansembe pamene padalembedwa mau akuti, ‘Kwa Mulungu wosadziŵika.’ Tsonotu amene mumampembedza osamdziŵayo, ndi yemweyo amene ine ndikukulalikirani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa potere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Chimene muchipembedza osachidziwa, chimenecho ndichilalikira kwa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti pamene ndimayenda ndi kuona zinthu zimene mumazipembedza, ndapezanso guwa lansembe lolembedwapo kuti, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Tsopano chimene mumachipembedza osachidziwa ndi chimene ndikuchilalikira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa potere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Cimene mueipembedza osacidziwa, cimeneco ndicilalikira kwa inu.