Acts 17:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono popeza kuti tili ngati ana a Mulungu, sitiyenera kuganiza kuti umulungu wake umafanafana ndi fano lagolide kapena lasiliva kapena lamwala, lopangidwa mwa luso ndi nzeru za munthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza tsono tili mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golide, kapena siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono popeza ndife ana a Mulungu, tisaganize kuti umulungu wake ndi wofanana ndi ndalama zagolide, zasiliva, mwala, kapenanso fanizo lopangidwa mwaluso la nzeru za anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza tsono tiri mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golidi, kapena siliva, kapena mwala, woloca ndi luso ndi zolingalira za anthu.