Acts 17:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa adaika tsiku pamene Iye adzaweruza anthu a pa dziko lonse lapansi molungama kudzera mwa Munthu amene Iye adamsankha. Adatsimikizira anthu onse zimenezi pakuukitsa Munthuyo kwa akufa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m'chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa Iye kwa akufa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Iye wayika tsiku limene adzaweruze dziko lapansi mwa chilungamo kudzera mwa Munthu amene anamusankha. Iye watsimikizira anthu onse zimenezi pomuukitsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m'cilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse citsimikizo, pamene anamuukitsa iye kwa akufa.