Acts 17:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Ayuda ena adachita nsanje, choncho adasonkhanitsa anthu opandapake ongoyendayenda, nayambitsa chipolowe mumzindamo. Adathamangira ku nyumba ya Yasoni, kukafuna Paulo ndi Silasi kuti aŵatulutsire ku anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa achabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nachititsa phokoso m'mudzi; ndipo anagumukira kunyumba ya Yasoni, nafuna kuwatulutsira kwa anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Ayuda ena anachita nsanje; kotero anasonkhanitsa anthu akhalidwe loyipa ochokera pa msika ndipo napanga gulu nayambitsa chipolowe mu mzindawo. Anathamangira ku nyumba ya Yasoni kukafuna Paulo ndi Sila kuti awabweretse pa gulu la anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa acabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nacititsa phokoso m'mudzi; ndipo anagumukira ku nyumba ya Yasoni, nafuna kuwaturutsira kwa anthu.