Acts 17:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Poona kuti sadaŵapeze, adamtenga Yasoniyo pamodzi ndi abale ena nkuŵaguzira kwa akulu amumzindamo. Tsono adafuula kuti, “Anthu aja amene akhala nasokoneza anthu ponseponse, tsopano afikanso kwathu kuno,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene sanawapeza anakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa akulu a mudzi, nafuula kuti, Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma atalephera kuwapeza, anakokera Yasoniyo ndi abale ena ku bwalo la akulu a mzindawo akufuwula kuti, “Anthu awa, Paulo ndi Sila, amene akhala akusokoneza dziko lonse lapansi, tsopano afikanso kuno.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene sanawapeza anakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa akuru a mudzi, napfuula kuti, Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso;