Acts 18:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamene Paulo adati azilankhula, Galio adauza Ayuda kuti, “Ukadakhala mlandu wakuti munthu wachimwira lamulo, kapena wakuti walakwira mnzake, bwenzi nditakumverani bwinobwino, Ayuda inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene Paulo anati atsegule pakamwa pake, Galio anati kwa Ayuda, Ukadakhala mlandu wa chosalungama, kapena dumbo loipa, Ayuda inu, mwenzi nditakumverani inu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Paulo ankati ayankhule, Galiyo anati kwa Ayuda, “Ukanakhala mlandu wochita choyipa kapena wolakwira mnzake, bwenzi nditakumverani bwinobwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene Paulo anati atsegule pakamwa pace, Galiyo anati kwa Ayuda, Ukadakhala mlandu wa cosalungama, kapena dumbo loipa, Ayuda inu, mwenzi nditakumverani inu;