Acts 18:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumeneko adapezako Myuda wina, dzino lake Akwila, mbadwa ya ku Ponto. Iye anali atangofika chatsopano kuchokera ku Italiya pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudio, Mfumu ya ku Roma, adaalamula kuti Ayuda onse achoke ku Roma. Tsono Paulo adapita kukaŵaona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapeza Myuda wina dzina lake Akwila, fuko lake la ku Ponto, atachoka chatsopano ku Italiya, pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudio analamulira Ayuda onse achoke m'Roma; ndipo Paulo anadza kwa iwo:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumeneko anakumana ndi Myuda wina dzina lake Akula, nzika ya ku Ponto amene anali atangofika kumene kuchokera ku Italiya pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudiyo analamula Ayuda onse kuti achoke ku Roma. Paulo anapita kukawaona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapeza Myuda wina dzina lace Akula, pfuko lace la ku Ponto, atacoka catsopano ku Italiya, pamodzi ndi mkazi wace Priskila, cifukwa Klaudiyo analamulira Ayuda onse acoke m'Roma; ndipo Pauloanadza kwa iwo: