Acts 18:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adayamba kulankhula molimba mtima m'nyumba yamapemphero ya Ayuda. Koma pamene Prisila ndi Akwila anamumva, adamtenga namufotokezera Njira ya Mulungu molongosoka koposa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Prisila ndi Akwila, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayamba kuyankhula mʼsunagoge molimba mtima. Pamene Prisila ndi Akula anamva, iwo anamuyitanira ku nyumba yawo ndipo anamufotokozera njira ya Mulungu molongosoka bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Priskila ndi Akula, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.