Acts 18:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Apolo adafuna kuwolokera ku Akaiya, abale adamlimbikitsa, nalembera ophunzira akumeneko kalata kuti amlandire bwino. Tsono atafikako, adaŵathandiza kwambiri amene anali atakhulupirira chifukwa cha kukoma mtima kwa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene iye anafuna kuoloka kunka ku Akaya, abale anamfulumiza, ndi kulembera akalata kwa ophunzira kuti amlandire: ndipo pamene anafika, iye anathangata ndithu iwo akukhulupirira mwa chisomo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Apolo anafuna kupita ku Akaya, abale anamulimbikitsa, nalemba kalata kwa ophunzira a kumeneko kuti amulandire. Atafika kumeneko, anathandiza kwambiri amene anakhulupirira mwachisomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene iye anafuna kuoloka kunka ku Akaya, abale anamfulumiza, ndi kulembera akalata kwa akuphunzira kuti amlandire: ndipo pamene anafika, iye anathangata ndithu iwo akukhulupira mwa cisomo;