Acts 18:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye popeza kuti iwo anali amisiri a ntchito imodzimodzi ngati yake, yosoka mahema, iyeyo adakhala nawo namagwirira limodzi ntchito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo popeza anali wa ntchito imodzimodzi, anakhala nao, ndipo iwowa anagwira ntchito; pakuti ntchito yao inali yakusoka mahema.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza Paulo anali mʼmisiri wosoka matenti monga iwo, iye anakhala nawo namagwirira ntchito pamodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo popeza anali wa nchito imodzimodzi, anakhala nao, ndipo iwowa anagwira nchito; pakuti nchito yao inali yakusoka mahema.