Acts 18:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pakuti iwo adaatsutsana naye ndi kumchita chipongwe, Paulo adalekana nawo pakukutumula zovala zake, naŵauza kuti, “Mwadziphetsa ndi mtima wanu. Tsono izo nzanu, ine ndilibe chifukwa. Kuyambira tsopano ndipita kwa akunja.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene iwo, anamkana, nachita mwano, anakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndilibe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene Ayuda anatsutsana naye ndi kumuchita chipongwe, iye anakutumula zovala zake nati, “Magazi anu akhale pamitu yanu! Ine ndilibe mlandu. Kuyambira tsopano ndipita kwa anthu a mitundu ina.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene iwo anamkana, nacita mwano, anakutumula maraya ace, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndiribe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.