Acts 19:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ankati akatenga zitambaya kapena nsalu zina zimene Paulo ankagwiritsa ntchito, nakaziika pa anthu odwala, odwalawo ankachira, ndipo mizimu yoipa inkatuluka mwa iwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsalu zopukutira ndi za pantchito, zochokera pathupi pake, ndipo nthenda zinawachokera, ndi ziwanda zinatuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero kuti mipango yopukutira thukuta ndi yovala pogwira ntchito, zomwe zinakhudza thupi la Paulo amapita nazo kwa odwala ndipo amachiritsidwa ndiponso mizimu yoyipa mwa iwo imatuluka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsaru zopukutira ndi za panchito, zocokera pathupi pace, ndipo nthenda zinawacokera, ndi mizimu yoipa inaturuka.