Acts 19:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Demetrioyo adasonkhanitsa anthu akewo, pamodzi ndi ena ogwira ntchito ya mtundu womwewo, naŵauza kuti, “Abale anga, mukudziŵa kuti chuma chathu chimachokera ku ntchito imeneyi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amenewo iye anawasonkhanitsa pamodzi ndi amisiri a ntchito yomweyo, nati, Amuna inu, mudziwa kuti ndi malonda awa ife tipeza chuma chathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anasonkhanitsa pamodzi amisiriwo, pamodzinso ndi anthu ena ogwira ntchito yomweyo ndipo anati, “Anthu inu, mukudziwa kuti ife timapeza chuma chathu kuchokera pa ntchito imeneyi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amenewo iye anawasonkhanitsa pamodzi ndi amisiri a nchito yomweyo, nati, Amuna inu, mudziwa kuti ndi malonda awa ife tipeza cuma cathu.