Acts 19:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono choopsa nchakuti ntchito yathuyi ifika ponyozeka. Si pokhapo ai, komanso nyumba yopembedzeramo Aritemi, mulungu wathu wamkulu, anthu sadzaiyesa kanthu. Ndiye basitu udzawonongeka ulemerero wonse wa Aritemiyo, amene anthu onse a ku Asiya ndi a pa dziko lonse lapansi amampembedza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo tiopa ife kuti ntchito yathuyi idzayamba kunyonyosoka; komanso kuti Kachisi wa mulungu wamkazi Aritemi adzayamba kuyesedwa wachabe; ndiponso kuti iye adzayamba kutsitsidwa ku ukulu wake, iye amene a m'Asiya onse, ndi onse a m'dziko lokhalamo anthu, ampembedza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choopsa ndi chakuti sikungowonongeka kwa ntchito yathu yokha ayi, komanso kuti nyumba ya mulungu wamkulu wamkazi Atemi idzanyozedwa ndipo mulungu wamkazi weniweniyo amene amapembedzedwa ku Asiya konse ndi dziko lapansi, ukulu wake udzawonongekanso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo tiopa ife kuti nchito yathuyi idzayamba kunyonyosoka; komanso kuti kacisi wa mlungu wamkazi Artemi adzayamba kuyesedwa wacabe; ndiponso kuti iye adzayamba kutsitsidwa ku ukulu wace, iye amene a m'Asiya onse, ndi onse a m'dziko lokhalamo anthu, ampembedza.