Acts 19:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Msonkhano wonse wa anthu aja udangoti pwirikiti: ena akufuula zina, enanso zina; ambiri osadziŵa ndi chimene asonkhanira chomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ena anafuula kanthu kena, ena kanthu kena; pakuti msonkhanowo unasokonezeka; ndipo unyinji sunadziwa chifukwa chake cha kusonkhana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munali chisokonezo mʼbwalomo pakuti ena amafuwula zina, enanso zina. Anthu ambiri sanadziwe ngakhale chomwe anasonkhanira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ena anapfuula kanthu kena, ena kanthu kena; pakuti msonkhanowo unasokonezeka; ndipo unyinji sunadziwa cifukwa cace ca kusonkhana.