Acts 19:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ena m'khamumo adaaganiza kuti Aleksandro alipo ndi chonena, ataona kuti Ayuda amkankhira kutsogolo. Tsono iye adakweza dzanja kuti aŵakhalitse chete, kuti afotokozere anthu mlanduwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatulutsa Aleksandro m'khamumo, kumtulutsa iye Ayuda. Ndipo Alesandro anatambasula dzanja, nafuna kudzikanira kwa anthu adasonkhanawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayuda anamukankhira Alekisandro kutsogolo, ndipo ena anafuwula kumulangiza iye. Iye anatambasula dzanja kuti anthu akhale chete kuti afotokozere anthu nkhaniyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaturutsa Alesandro m'khamumo, kumturutsa iye Ayuda. Ndipo Alesandro anatambasula dzanja, nafuna kudzikanira kwa anthu adasonkhanawo.