Acts 19:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamene anthu aja adazindikira kuti iyeyo ndi Myuda, onsewo adafuula pamodzi pa maola aŵiri kuti, “Ndi wamkulu Aritemi wa Aefeso!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pozindikira kuti ali Myuda, kunali mau amodzi a kwa onse akufuula monga maora awiri, Wamkulu ndi Aritemi wa Aefeso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene anthuwo anazindikira kuti ndi Myuda, onse pamodzi kwa maora awiri anafuwula kuti, “Wamkulu ndi Atemi wa ku Efeso!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pozindikira kuti ali Myuda, kunali mau amodzi a kwa onse akupfuula monga maora awiri, Wamkuru ndi Artemi wa Aefeso.