Acts 19:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mlembi wa mzindawo ataŵatontholetsa anthu aja, adaŵauza kuti, “Inu Aefeso, ndani amene sadziŵa kuti mzinda wa Aefeso ndiwo wosunga nyumba yopembedzeramo Aritemi wamkulu, ndiponso wosunga mwala wopatulika uja umene udachita kugwa kuchokera kumwamba?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene mlembi adatontholetsa khamulo, anati, Amuna a Efeso inu, munthuyu ndani wosadziwa kuti mudzi wa Aefeso ndiwo wosungira Kachisi wa Aritemi wamkulu, ndi fano lidachokera kwa Zeusi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mlembi wa mzindawo anakhazikitsa bata gulu la anthuwo ndipo anati, “Anthu a ku Efeso, kodi ndani pa dziko lonse lapansi amene sadziwa kuti mzinda wa Efeso umayangʼanira nyumba ya mulungu wamkulu Atemi ndi fanizo lake, limene linagwa kuchokera kumwamba?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene mlembi adatontholetsa khamulo, anati, Amuna a Efeso inu, munthuyu ndani wosadziwa kuti mudzi wa Aefeso ndiwo wosungira kacisi wa Artemi wamkuru, ndi fano Iidacokera kwa Zeu?