Acts 19:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ena adaumitsa mitima yao, osafuna kukhulupirira, nkumanyoza Njira ya Ambuye pamaso pa gulu lonse. Pamenepo Paulo adaŵasiya nachoka nawo ophunzira aja, ndipo tsiku ndi tsiku ankakambirana m'sukulu ya Tirano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo pamaso pa anthu, anawachokera, napatutsa ophunzira, nafotokozera masiku onse m'sukulu ya Tirano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ena anawumitsa mitima; anakana kukhulupirira ndipo ananyoza Njirayo pa gulu la anthu. Kotero Paulo anawasiya. Iye anatenga ophunzirawo ndipo amakambirana tsiku ndi tsiku mʼsukulu ya Turano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo pamaso pa anthu, anawacokera, napatutsa akuphunzira, nafotokozera masiku onse m'sukulu ya Turano.