Acts 2:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“ ‘Mulungu akuti, Pa masiku otsiriza ndidzaika Mzimu wanga mwa anthu onse, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi azidzalalika za Mulungu. Anyamata anu azidzaona zinthu m'masomphenya, ndipo nkhalamba zanu zizidzalota maloto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Mulungu akuti, mʼmasiku otsiriza ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse. Ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera, anyamata anu adzaona masomphenya, nkhalamba zanu zidzalota maloto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, Ndidzathira ca Mzimu wansa pa thupi liri lonse, Ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera, Ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, Ndi akulu anu adzalota maloto;