Acts 2:45 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ankagulitsa minda yawo ndi katundu wawo, ndi kugawira kwa aliyense molingana ndi zosowa zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zimene anali nazo, ndi cuma cao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.