Acts 20:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tidachokanso kumeneko m'chombo, ndipo m'maŵa mwake tidakafika pafupi ndi Kiyo. M'maŵa mwakenso tidawolokera ku Samo, ndipo mkucha wake tidakafika ku Mileto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene tidachokerapo, m'mawa mwake tinafika pandunji pa Kiyo; ndi m'mawa mwake tinangokocheza ku Samo, ndi m'mawa mwake tinafika ku Mileto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa mwake tinachoka kumeneko pa sitima ya pamadzi ndipo tinafika pafupi ndi Kiyo. Tsiku linalo tinawolokera ku Samo, ndipo tsiku linanso tinafika ku Mileto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene tidacokerapo, m'mawa mwace tinafika pandunjipa Kiyo; ndi m'mawa mwace tinangokoceza ku Samo, ndi m'mawa mwace tinafika ku Mileto.