Acts 20:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukudziŵa kuti sindidakubisireni kanthu kalikonse koti nkukuthandizani. Ndidakulalikirani ndi kukuphunzitsani poyera ndiponso m'nyumba zanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m'nyumba zanu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mukudziwa kuti, sindinakubisireni kanthu kalikonse kopindulitsa koma ndinakuphunzitsani poyera komanso nyumba ndi nyumba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m'nyumba m'nyumba,