Acts 20:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye inu khalani maso. Kumbukirani kuti pa zaka zitatu usana ndi usiku sindidaleke kulangiza aliyense mwa inu ndi misozi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake dikirani, nimukumbukire kuti zaka zitatu sindinaleka usiku ndi usana kuchenjeza yense wa inu ndi misozi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono inu, samalani! Kumbukirani kuti kwa zaka zitatu, usana ndi usiku ndiponso ndi misozi sindinaleke kuchenjeza aliyense wa inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace dikirani, nimukumbukile kuti zaka zitatu sindinaleka usiku ndi usana kucenjeza yense wa inu ndi misozi.