Acts 20:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Makamaka adachita chisoni chifukwa cha mau ake aja onena kuti iwo sadzaonanso nkhope yake. Pambuyo pake adamperekeza kuchombo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nalira makamaka chifukwa cha mau adanenawa, kuti sadzaonanso nkhope yake. Ndipo anamperekeza iye kungalawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chimene chinamvetsa chisoni kwambiri ndi mawu ake akuti sadzaonanso nkhope yake. Kenaka iwo anamuperekeza ku sitima yapamadzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nalira makamaka cifukwa ca mau adanenawa, kuti sadzaonanso nkhope yace. Ndipo anamperekeza iye kungalawa.