Acts 20:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ife tidayenda pa chombo kuchokera ku Filipi, itatha Paska, chikondwerero cha mikate yosafufumitsa. Ndipo patapita masiku asanu, tidakumana nawo ku Troasi. Kumeneko tidakhalako masiku asanu ndi aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tinapita m'ngalawa kuchokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda chotupitsa, ndipo popita masiku asanu tinawapeza ku Troasi; pamenepo tinatsotsa masiku asanu ndi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ife tinayenda pa sitima ya pamadzi kuchokera ku Filipi chitatha Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. Patapita masiku asanu tinakumana nawo enawo ku Trowa, ndipo tinakhala kumeneko masiku asanu ndi awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tinapita m'ngalawa kucokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda cotupitsa, ndipo popita masiku asanu tinawapeza ku Trowa; pamenepo tinatsotsa masiku asanu ndi awiri.