Acts 20:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku loyamba la sabata, tidasonkhana kuti tidye Mgonero, ndipo Paulo ankakamba ndi anthu. Popeza kuti ankayembekeza kupita m'maŵa mwake, adapitiriza kulankhula mpaka pakati pa usiku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati achoke m'mawa mwake; ndipo ananena chinenere kufikira pakati pa usiku.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku loyamba la Sabata, tinasonkhana kuti tidye mgonero. Paulo analalikira kwa anthu chifukwa anaganiza zoti achoke tsiku linalo, ndipo analalika mpaka pakati pa usiku.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati acoke m'mawa mwace; ndipo ananena cinenere kufikira pakati pa usiku.