Acts 20:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mnyamata wina, dzina lake Yutiko, adaakhala pa windo. Tsono Paulo akukambabe ndi anthu aja, Yutikoyo ankaodzera kwambiri, mpaka adagona tulo ndithu, nagwa pansi kuchokera pa nyumba yam'mwamba. Ndipo adamtola ali wakufa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mnyamata dzina lake Yutiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikulu; ndipo pakukhala chifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja pachiwiri, ndipo anamtola wakufa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa chipinda chachitatu chammwamba cha nyumbayo, pa zenera, panakhala mnyamata wina dzina lake Utiko, amene ankasinza pomwe Paulo amayankhulabe. Atagona tulo, iye anagwa pansi kuchokera pa chipinda chammwamba ndipo anamutola atafa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mnyamata dzina lace Utiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikuru; ndipo pakukhala cifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja paciwiri, ndipo anamtola wakufa.