Acts 21:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Titalaŵirana nawo, tidachoka kumeneko m'chombo, ndipo tidayenda molunjika kukafika ku Kosi. M'maŵa mwake tidakafika ku Rode, ndipo kuchokera kumeneko tidakafika ku Patara.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, titalekana nao ndi kukankha ngalawa, tinadza molunjika ku Kosi, ndi m'mawa mwake ku Rode, ndipo pochokerapo ku Patara;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Titalawirana nawo, tinachoka kumeneko mʼsitima ya pamadzi, ndipo tinayenda molunjika mpaka kufika ku Kosi. Mmawa mwake tinapita ku Rode, kuchokera kumeneko tinapita ku Patara.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, titalekana nao ndi kukankha ngalawa, tinadza molunjika ku Ko, ndi m'mawa mwace ku Rode, ndipo pocokerapo ku Patara;