Acts 21:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ophunzira ena a ku Kesareya nawonso adatsagana nafe. Adakatitula kunyumba kwa munthu wina, dzina lake Mnasoni, kumene adaakonza kuti tizikakhala. Iyeyu anali wa ku Kipro, ndipo anali wophunzira wakalekale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamuka nafenso ena a ophunzira a ku Kesareya, natenganso wina Mnasoni wa ku Kipro, wophunzira wakale, amene adzatichereza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ena mwa ophunzira a ku Kaisareya anatiperekeza mpaka kukatifikitsa ku nyumba ya Mnasoni, kumene tinakonza kuti tizikhalako. Iye anali wa ku Kupro ndiponso mmodzi wa ophunzira oyambirira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamuka nafenso ena a ophunzira a ku Kaisareya, natenganso wina Mnaso wa ku Kupro, wophunzira wakale, amene adzaticereza.