Acts 21:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene iwo adamva zimenezi, adayamika Mulungu. Ndipo adauza Paulo kuti, “Inu mbale wathu, mukuwona kuti pali Ayuda ambirimbiri amene asanduka okhulupirira. Onsewo ngokhulupirika kwambiri pa kutsata Malamulo a Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupirira; ndipo ali nacho changu onsewa, cha pa chilamulo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atamva zimenezi, iwo anayamika Mulungu. Kenaka anawuza Paulo kuti, “Mʼbale, ukuona kuti pali Ayuda ambirimbiri amene anakhulupirira, ndipo ndi okhulupirika potsatira Malamulo a Mose.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupira; ndipo ali naco cangu onsewa, ca pa cilamulo;