Acts 21:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muŵatenge ndipo muchite nawo mwambo wakudziyeretsa. Tsono muŵalipirire zoti apereke ku Nyumba ya Mulungu kuti amete tsitsi lao. Mukatero, anthu onse adzadziŵa kuti si zoona zimene anthu adaŵauza za inu, koma kuti inu mumasamala ndithu Malamulo a Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amenewa uwatenge nudziyeretse nao pamodzi, nuwalipirire, kuti amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzachabe, koma kuti iwe wekhanso uyenda molunjika, nusunga chilamulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muwatenge anthu amenewa, ndipo muchite nawo mwambo wowayeretsa ndipo muwalipirire zoti apereke kuti amete tsitsi lawo. Kotero aliyense adzadziwa kuti palibe choonadi pa zimene anamva za inu, koma kuti inu mwini mumakhala moyo womvera Malamulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amenewa uwatenge nudziyeretse nao pamodzi, nuwalipirire, kati amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzacabe, koma kuti iwe wekhaoso uyenda molunjika, nusunga cilamulo.