Acts 21:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kunena za anthu a mitundu ina amene adasanduka okhulupirira, ife taŵalembera kalata yoŵauza zimene tidavomerezana: kuti asamadye chakudya chimene chidaperekedwa nsembe ku mafano, asamadye magazi kapena nyama yochita kupotola, ndiponso asamachite dama.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kunena za amitundu adakhulupirirawo, tinalembera ndi kulamulira kuti asale zoperekedwa kwa mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma kunena za anthu a mitundu ina amene asandulika okhulupirira, ife tinawalembera zimene tinavomerezana zakuti asadye chakudya choperekedwa ku mafano, asadye magazi, asadye nyama yopotola ndiponso asachite zadama.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kama kunena za amitundu adakhulupirawo, tinalembera ndi kulamulira kuti asale zoperekedwa kwa mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama.