Acts 21:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Paulo adaŵatenga anthu anai aja, ndipo m'maŵa mwake adachita nawo mwambo wakudziyeretsa. Iyeyo adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu nakadziŵitsa ansembe za tsiku loti aliyense mwa iwo adzamperekere nsembe, atatha masiku akudziperekawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m'mawa mwake m'mene anadziyeretsa nao pamodzi, analowa m'Kachisi, nauza chimalizidwe cha masiku a kuyeretsa, kufikira adawaperekera iwo onse mtulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa mwake Paulo anatenga amuna aja ndipo anachita mwambo wodziyeretsa. Kenaka anapita ku Nyumba ya Mulungu nakadziwitsa ansembe za tsiku limene adzatsiriza nthawi ya kudziyeretsa ndi kuperekera nsembe aliyense wa iwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m'mawa mwace m'mene anadziyeretsa nao pamodzi, analowa m'Kacisi, nauza cimarizidwe ca masiku a kuyeretsa, kufikira adawaperekera iwo onse mtulo.