Acts 21:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atatha masiku asanu ndi aŵiri aja, Ayuda ochokera ku Asiya adaona Paulo m'Nyumba ya Mulungu. Adautsa mitima ya anthu onse, namgwira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene masiku asanu ndi awiri anati amalizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye m'Kachisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ali pafupi kutsiriza masiku asanu ndi awiriwo, Ayuda ena ochokera ku Asiya anaona Paulo mʼNyumba ya Mulungu. Iwo anawutsa gulu lonse la anthu ndipo anamugwira Paulo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene masiku asanu, ndi awiri anati amarizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye m'Kacisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira,