Acts 21:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iwo adafuula kuti, “Inu Aisraele, tithandizeni! Ndi uyutu munthu uja amene akuphunzitsa anthu ponseponse zonyoza mtundu wathu, Malamulo a Mose ndiponso malo ano. Kuwonjezera apo waloŵetsanso akunja m'Nyumba ya Mulungu muno, ndi kudetsa malo athu opatulikaŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nafuula, Amuna a Israele, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi chilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Agriki nalowa nao m'Kachisi, nadetsa malo ano oyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
akufuwula kuti, “Inu Aisraeli, tithandizeni! Ndi uyu munthu uja amaphunzitsa anthu onse ponseponse kuti azinyoza mtundu wathu ndiponso Malamulo athu ndi malo ano. Kuwonjezera pamenepo, walowetsa Agriki mʼbwalo la Nyumba ino ndipo wadetsa malo opatulika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
napfuula, Amuna a Israyeli, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi cilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Ahelene nalowa nao m'Kacisi, nadetsa malo ana oyera.